Amos 9

Israeli Adzawonongedwa

1Ine ndinaona Ambuye atayima pambali pa guwa lansembe, ndipo anati:

“Kantha mitu ya nsanamira
kuti ziwundo za nyumba zigwedezeke.
Muzigwetsere pa mitu ya anthu onse,
onse amene atsalira ndidzawapha ndi lupanga.
Palibe ndi mmodzi yemwe amene adzathawe,
palibe amene adzapulumuke.
2Ngakhale atakumba pansi mpaka ku malo a anthu akufa,
dzanja langa lidzawatulutsa kumeneko.
Ngakhale atakwera kumwamba
Ine ndidzawatsakamutsa kumeneko.
3Ngakhale atakabisala pamwamba pa phiri la Karimeli,
Ine ndidzawasaka kumeneko ndi kuwagwira.
Ngakhale atakabisala pansi pa nyanja yayikulu,
ndidzalamula njoka kuti iwalume kumeneko.
4Ngakhale adani awo awakusire ku ukapolo,
ndidzalamula lupanga kuti liwaphe kumeneko.
Ndidzawayangʼanitsitsa
kuti zoyipa ziwagwere; osati zabwino.”

5Ambuye Yehova Wamphamvuzonse
amene amakhudza dziko lapansi ndipo dzikolo limasungunuka,
onse amene amakhala mʼmenemo amalira.
Dziko lonse lidzadzaza ngati mtsinje wa Nailo,
kenaka nʼkuphwera ngati mtsinje wa ku Igupto.
6Iye amene amamanga malo ake okhalamo kumwamba,
ndi kuyika maziko ake pa dziko lapansi,
Iye amene amayitana madzi a ku nyanja
ndikuwakhuthulira pa dziko lapansi,
dzina lake ndiye Yehova.

7“Kodi kwa Ine, inu Aisraeli, simuli
chimodzimodzi ndi Akusi?”
Akutero Yehova.
“Kodi sindine amene ndinatulutsa Israeli ku Igupto,
Afilisti ku Kafitori
ndi Aaramu ku Kiri?

8“Taonani, maso a Ambuye Yehova
ali pa ufumu wochimwawu.
Ndidzawufafaniza
pa dziko lapansi.
Komabe sindidzawononga kotheratu
nyumba ya Yakobo,”
akutero Yehova.
9“Pakuti ndidzalamula,
ndipo ndidzagwedeza nyumba ya Israeli
pakati pa mitundu yonse ya anthu
monga momwe amasefera ufa mʼsefa,
koma palibe nʼkamwala kamodzi komwe kamene kadzagwe pansi.
10Anthu onse ochimwa pakati pa anthu anga
adzaphedwa ndi lupanga,
onse amene amanena kuti,
‘Tsoka silidzatigwera ife kapena kutiwononga.’

Kubwezeretsedwa kwa Israeli

11“Tsiku limenelo ndidzabwezeretsa
nyumba ya Davide imene inagwa.
Ndidzakonzanso malo amene anagumuka,
ndi kuyimanganso
monga inalili poyamba,
12kuti adzatengenso otsala a Edomu
ndi mitundu yonse imene imatchedwa ndi dzina langa,”
akutero Yehova amene adzachita zinthu izi.
13Yehova akunena kuti

“Nthawi ikubwera pamene mlimi wotipula adzapyola wokolola
ndipo woponda mphesa adzapyola wodzala mbewu.
Mapiri adzachucha vinyo watsopano
ndi kuyenderera pa zitunda zonse.
14Ndidzawabwezeranso pabwino anthu anga Aisraeli;
mizinda imene inali mabwinja idzamangidwanso ndipo azidzakhalamo.
Adzalima minda ya mpesa ndipo adzamwa vinyo wake;
adzalima minda ndipo adzadya zipatso zake.
15Ndidzakhazika Aisraeli mʼdziko mwawo,
ndipo sadzachotsedwamonso mʼdziko
limene Ine ndawapatsa,”

akutero Yehova Mulungu wako.
Copyright information for NyaCCL